Mark 14:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adabwerako kachitatu, adati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Basi tsopano. Nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akuperekedwa kwa anthu ochimwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a anthu ochimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza kacitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; cakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu ocimwa.