Mark 14:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu akulankhula choncho, nthaŵi yomweyo wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo, Iye ali chilankhulire, anadza Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ochokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo, Iye ali cilankhulire, anadza Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ocokera kwa ansembe akuru ndi alembi ndi akuru.