Mark 14:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma izi zatere kuti zipherezere zomwe Malembo adanena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku onse ndinali nanu m'Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwanitsidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku onse ndinali nanu m'Kacisi ndirikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ici cacitika kuti malembo akwanitsidwe.