Mark 14:58 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Munthu uyu ife tidamumva akunena kuti, ‘Ine ndidzapasula Nyumba ya Mulunguyi, yomangidwa ndi anthu chabe, ndipo patapita masiku atatu ndidzamanga ina yosamangidwa ndi anthu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kacisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.