Mark 14:65 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m'maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti, “Lotatu, wakumenya ndani?” Alonda aja nawonso adayamba kummenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ena mayamba kumthira malobvu Iye, adi kuphimba nkhope yace, ndi cumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo ananpanda Iye kofu.