Mark 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, kotero kuti pamene mufuna kuŵachitira zachifundo, mungathe kuŵachitira. Koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo pali ponse pamene mukafuna mukhoza kuwacitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.