Mark 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chonkumbukira nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino ku dziko lonse lapansi, icinso cimene anacita mkazi uyu cidzanenedwa, cikhale comkumbukira naco.