Mark 15:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa njira adakumana ndi munthu wina, amene ankadutsa pamenepo kuchokera ku midzi. Munthuyo anali Simoni wa ku Kirene, bambo wake wa Aleksandro ndi Rufu. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakangamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, atate wao wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wace.