Mark 15:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira!” Ndiponso amene adaŵapachika pamodzi naye aja ankamunyoza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atsike tsopano pamtanda, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupacikidwa naye anamlalatira.