Mark 15:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero wina adathamanga nakaviika chinkhupule m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Anzakewo adati, “Taima, tiwone ngati Eliyayo abweredi kudzamtsitsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anathamanga wina, nadzaza cinkhupule ndi vinyo wosasa naciika pabango, namwetsa Iye nanena, Lekani; tione ngati Eliys adza kudzamtsitsa.