Mark 16:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe, ndiponso Salome adakagula zonunkhira kuti akadzoze mtembo wa Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo litapita Sabata, Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.