Mark 16:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potsiriza Yesu adaonekera ophunzira khumi ndi mmodzi aja alikudya. Adaŵadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwao ndi kupulupudza kwao, chifukwa sadakhulupirire anzao aja amene adaamuwona Iye atauka kwa akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo citatha ico anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pacakudya; ndipo anawadzudzula cifukwa ca kusabvomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanabvomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.