Mark 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo azimaiwo adatuluka nkuthaŵako kumandako, popeza kuti adaagwidwa ndi mantha, mpaka kumangonjenjemera. Ndipo chifukwa cha manthawo sadauze munthu aliyense kanthu. [
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha. [Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe vesi 9 mpaka 20.]
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukuru kudawagwira; ndipo sanauza kanthu kwa munthu ali yense; pakuti anacitamantha.