Mark 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu uja adadzukadi, natenga machira ake aja nkutuluka, onse aja akuwona. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu nkumanena kuti, “Zoterezi ife sitinaziwone nkale lonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, naturuka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.