Mark 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankayenda, adaona Levi, mwana wa Alifeyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumuka, anaona Levi mwana wa Alifeyu alikukhala polandira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.