Mark 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba mwa Leviyo, panali anthu ambiri okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa, odzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Anali anthu ambiri ndithu amene adaatsagana naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwace, ndipo amisonkho ndi ocimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.