Mark 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene aphunzitsi a Malamulo a m'gulu la Afarisi adaona kuti Yesu akudya ndi anthu ochimwa, ndiponso ndi anthu okhometsa msonkho, adafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ocimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ace, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ocimwa.