Mark 2:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina ophunzira a Yohane Mbatizi ndiponso Afarisi ankasala zakudya. Anthu adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala zakudya, koma ophunzira anu ai?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?