Mark 2:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Suja adaaloŵa m'nyumba ya Mulungu, pa nthaŵi imene Abiyatara anali mkulu wa ansembe onse, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo nkosaloledwa kuti wina aliyense nkumudya, kupatula ansembe okha. Komanso adaagaŵirako anzake aja amene adaali naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuti, analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?