Mark 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma sadathe kufika naye pafupi ndi Yesuyo chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho adakwera pa denga, nangosasula dengalo kuyang'anana ndi pamene Yesu analiri, nkutsitsira pachiboopo machira amene adaanyamulira munthu uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene sanakhoza kufika kuli Iye, cifukwa ca khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo,