Mark 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chapafupi koposa nchiti, kumuuza wa ziwalo zakufayu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, nyamula machira ako, yamba kuyenda?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Capafupi nciti, kapena kuuza wodwala manjenje kuti, Macimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?