Mark 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizimu yoipa inkati ikamuwona, inkadzigwetsa pansi pafupi ndi Iye nkumafuula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nipfuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.