Mark 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankangomuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthuyo pa tsiku la Sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamciritsa dzuwa la Sabata; kuti ammange mlandu.