Mark 3:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu.” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Beelzibule, ndipo, Ndi mkuru wao wa ziwanda aturutsa ziwanda.