Mark 3:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Wina sangathe kungoloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m'nyumba mwakemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nvumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ace, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwace.