Mark 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adafunsa anthuwo kuti, “Kodi pa tsiku la Sabata chololedwa nchiti? Kuchitira anthu zabwino, kapena kuŵachita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” Anthuwo adangoti chete.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa dzuwa la Sabata kucita zabwino, kapena zoipa? kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala cete.