Mark 3:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ake anali a ku Galileya, ena a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu, ena a ku Idumeya, ndi kutsidya kwa Yordani, ndiponso kudera la ku Tiro ndi ku Sidoni. Onsewo adaafika kwa Iye, chifukwa anali atamva zimene Iye ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Y ordano, ndi a kufupi ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikuru, pakumva zazikuruzo anazicita, linadza kwa Iye.