Mark 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adayambanso kuphunzitsa pambali pa Nyanja ya Galileya. Anthu ochuluka adasonkhana kumeneko, kotero kuti Iye adaayenera kuloŵa m'chombo, nakhala pansi m'menemo panyanjapo. Anthu onse adaakhala pansi pa mtunda m'mphepete mwa nyanjayo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja, Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikurukuru, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.