Mark 4:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akaifesa, imamera, mbeu yake nkukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse. Imachita nthambi zazikulu, kotero kuti mbalame zimatha kudzamanga zisa mumthunzi mwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nichita nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nicita nthambi zazikuru; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwace.