Mark 4:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwo adasiya khamu la anthu lija, natenga Yesu m'chombo momwe adaalimo. Padaalinso zombo zina zotsagana naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.