Mark 4:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nthaŵi imeneyo Yesu anali kumbuyo m'chombomo, ali m'tulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?