Mark 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anailolao Ndipo mizimu yonyansa inaturuka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.