Mark 5:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Ataona Yesu, adadzigwetsa ku mapazi ake,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadzako mmodzi wa akuru a sunagoge, dzina lace Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ace, nampempha kwambiri,