Mark 5:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osacira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yace idakula,