Mark 5:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mkaziyo anacita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa cimene anamcitira iye, nadza, namgwadira, namuuza coona conse.