Mark 5:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mene iye ali cilankhulire, anafika a ku nyumba ya mkuru wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; ubvutiranjinso Mphunzitsi?