Mark 5:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye ataloŵa, adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafa, koma ali m'tulo.