Mark 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale anthu adaayesa kangapo kummanga miyendo ndi zitsulo, ndiponso kummanga manja ndi maunyolo, koma iye ankangoŵamwetsula maunyolowo, ndipo zitsulo zomanga miyendozo ankangozithyola. Padaalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumgonjetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti adafomangidwa kawiri kawiri ndi matangadza ndimaunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.