Mark 5:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adaŵatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkuloŵa kuchipinda kumene kunali mwana uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anamuseka Iye. Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamseka Iye pwepwete, Koma Iye anawaturutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amace, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.