Mark 5:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti zimenezo wina aliyense asazidziŵe. Kenaka adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ici munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.