Mark 6:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, nakana kumva mau anu, pochoka musanse fumbi la kumapazi kwanu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro choti apalamula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakucoka kumeneko, sansani pfumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.