Mark 6:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Herode adaazimva zimenezi, pakuti mbiri ya Yesu inali itamveka ponseponse. Anthu ena ankati, “Yohane Mbatizi uja adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace mphamvu izi zicitacita mwa Iye.