Mark 6:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Ndiye kuti Herode anali atamkwatira maiyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, cifukwa ca Herodiya, mkazi wa Filipo mbale wace; cifukwa adamkwatira iye.