Mark 6:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, Herodiasi adapezerapo mwai. Herodeyo adakonza phwando, naitana akuluakulu a Boma, ndi akulu olamulira asilikali, ndi anthu omveka a ku Galileyako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwace kwa Herode, iye anawakonzera phwando akuru ace ndi akazembe ace ndi anthu omveka a ku Galileya;