Mark 6:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwana wamkazi wa Herodiasi adaloŵa, nayamba kuvina. Kuvinako adakondweretsa nako kwambiri Herode ndi amene adaali naye paphwandopo. Pamenepo mfumuyo idauza mtsikanayo kuti, “Undipemphe chilichonse chimene ukufuna, ine ndikupatsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo. Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiya analowa yekha nabvina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pacakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine ciri conse ucifuna, ndidzakupatsa iwe.