Mark 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtsikana uja adabwerera msanga kwa mfumu nanena kuti, “Ndifuna kuti tsopano pompano mundipatse mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo analowa m'mangu m'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wace wa Yohane Mbatizi mumbizi.