Mark 6:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho nthaŵi yomweyo adatuma mmodzi mwa asilikali ake, namulamula kuti abwere nawo mutu wa Yohanewo. Msilikaliyo adapita ku ndende, nakamdula mutu Yohaneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wace; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende;