Mark 6:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ameneyu si mmisiri wa matabwa uja, mwana wa Maria? Kodi abale ake si Yakobe, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Kodi suja alongo ake ali nafe pompano?” Choncho adakhumudwa naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.