Mark 6:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵauza kuti, “Tiyeni tipite kwatokha kumalo kosapitapita anthu, kuti mukapumule pang'ono.” Adaatero chifukwa anthu anali piringupiringu, mwakuti iwo sankatha kupeza ndi mpata wodyera womwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.