Mark 6:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe anthu ambiri adaŵaona akupita, naŵazindikira. Motero adathamanga pa mtunda kuchokera ku mizinda yonse, nakafika kumaloko, Yesu ndi ophunzira ake aja asanafike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m'midzi monse, nawapitirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira.